ngakhale lisanade dzuwa, ndi kuunika, ndi mwezi, ndi nyenyezi, mitambo ndi kubweranso italeka mvula;
Yoweli 3:15 - Buku Lopatulika Dzuwa ndi mwezi zada, ndi nyenyezi zibweza kuwala kwao. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Dzuwa ndi mwezi zada, ndi nyenyezi zibweza kuwala kwao. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Dzuŵa ndi mwezi zada, ndipo nyenyezi zaleka kuŵala. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Dzuwa ndi mwezi zidzadetsedwa, ndipo nyenyezi sizidzawalanso. |
ngakhale lisanade dzuwa, ndi kuunika, ndi mwezi, ndi nyenyezi, mitambo ndi kubweranso italeka mvula;
Chifukwa nyenyezi za kumwamba ndi makamu ao sizidzawala; dzuwa lidzada m'kutuluka kwake, ndipo mwezi sudzaonetsa kuwala kwake.
Ndipo pakukuzima iwe ndidzaphimba thambo, ndi kudetsa nyenyezi zake; ndidzaphimba dzuwa ndi mtambo, ndi mwezi sudzaonetsa kuwala kwake.
Dziko lapansi linjenjemera pamaso pao, thambo ligwedezeka, dzuwa ndi mwezi zada, ndi nyenyezi zibweza kuwala kwao;
Dzuwa lidzasanduka mdima, ndi mwezi udzasanduka mwazi, lisanadze tsiku la Yehova lalikulu ndi loopsa.
Koma pomwepo, atapita masauko a masiku awo, dzuwa lidzadetsedwa, ndi mwezi sudzaonetsa kuwala kwake, ndi nyenyezi zidzagwa kuchokera kumwamba, ndi mphamvu za kumwamba zidzagwedezeka:
Koma m'masikuwo, chitatha chisautso chimenecho, dzuwa lidzadetsedwa, ndi mwezi sudzapatsa kuunika kwake,
Ndipo mngelo wachinai anaomba lipenga, ndipo limodzi la magawo atatu a dzuwa linagwidwa, ndi limodzi la magawo atatu a mwezi, ndi limodzi la magawo atatu a nyenyezi; kuti limodzi la magawo ao atatu lidetsedwe, ndi kuti limodzi la magawo ake atatu a usana lisawale, ndi usiku momwemo.