ndipo anayang'anira ku Sodomu ndi ku Gomora ndi ku dziko lonse la chigwa, ndipo anapenya, taonanitu, utsi wa dzikolo unakwera, monga utsi wa ng'anjo.
Yoweli 2:30 - Buku Lopatulika Ndipo ndidzaonetsa zodabwitsa kuthambo ndi padziko lapansi, mwazi, ndi moto, ndi utsi tolo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ndidzaonetsa zodabwitsa kuthambo ndi pa dziko lapansi, mwazi, ndi moto, ndi utsi tolo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Mu mlengalenga ndi pa dziko lapansi ndidzaonetsa zodabwitsa izi: magazi, moto ndi utsi watoloo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndidzaonetsa zodabwitsa mlengalenga ndi pa dziko lapansi, ndizo magazi, moto ndi utsi watolotolo. |
ndipo anayang'anira ku Sodomu ndi ku Gomora ndi ku dziko lonse la chigwa, ndipo anapenya, taonanitu, utsi wa dzikolo unakwera, monga utsi wa ng'anjo.
Ndaniyu akwera kutuluka m'chipululu ngati utsi wa tolo, wonunkhira ndi mure ndi lubani, ndi zonunkhiritsa zonse za wogulitsa?
Chifukwa chimenecho dziko lidzalira maliro, ndipo kumwamba kudzada; chifukwa ndanena, ndatsimikiza mtima, sindinatembenuka, sindidzabwerera pamenepo.
Koma pomwepo, atapita masauko a masiku awo, dzuwa lidzadetsedwa, ndi mwezi sudzaonetsa kuwala kwake, ndi nyenyezi zidzagwa kuchokera kumwamba, ndi mphamvu za kumwamba zidzagwedezeka:
ndipo kudzakhala zivomezi zazikulu, ndi njala ndi miliri m'malo akutiakuti, ndipo kudzakhala zoopsa ndi zizindikiro zazikulu zakumwamba.
Pamene amuna a ku Ai anacheuka, anapenya, ndipo taonani, utsi wa mzinda unakwera kumwamba; nasowa mphamvu iwo kuthawa chakuno kapena chauko; ndi anthu othawira kuchipululu anatembenukira owapirikitsa.
Ndipo mafumu a dziko ochita chigololo nadyerera naye, adzalira nadzaulira maliro pamene aona utsi wa kutentha kwake, poima patali,
Ndipo woyamba anaomba lipenga, ndipo panakhala matalala ndi moto, zosakaniza ndi mwazi, ndipo anazitaya padziko lapansi; ndipo limodzi la magawo atatu a dziko lidapserera, ndipo limodzi la magawo atatu a mitengo lidapserera, ndipo msipu wonse udapserera.
Koma kunali chizindikiro choikika pakati pa amuna a Israele ndi olalirawo, ndicho chakuti afukitse mtambo wa utsi kumzinda.
Koma pamene mtambo unayamba kukwera m'mzinda ngati utsi uli tolo, Abenjamini anacheuka, ndipo taonani, pamodzi ponse panafuka utsi kumwamba.