Nati Hazaele, Koma nanga kapolo wanu ali chiyani, ndiye galu, kuti akachite chinthu chachikulu ichi? Nayankha Elisa, Yehova wandionetsa kuti udzakhala mfumu ya pa Aramu.
Yoweli 2:20 - Buku Lopatulika koma ndidzakuchotserani kutali nkhondo ya kumpoto, ndi kulingira kudziko louma ndi lopasuka, a kumaso kwake kunyanja ya kum'mawa, ndi a kumbuyo kwake kunyanja ya kumadzulo; ndi kununkha kwake kudzakwera, ndi fungo lake loipa lidzakwera; pakuti inachita zazikulu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 koma ndidzakuchotserani kutali nkhondo ya kumpoto, ndi kulingira kudziko louma ndi lopasuka, a kumaso kwake kunyanja ya kum'mawa, ndi a kumbuyo kwake kunyanja ya kumadzulo; ndi kununkha kwake kudzakwera, ndi fungo lake loipa lidzakwera; pakuti inachita zazikulu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndidzachotsa adani akumpoto kuti akhale kutali ndi inu, ndipo ndidzaŵapirikitsira ku dziko louma ndi lachipululu. Akutsogolo ndidzaŵathamangitsira ku nyanja yakuvuma, akumbuyo ndidzaŵathamangitsira ku nyanja yakuzambwe. Tsono mitembo yao idzatulutsa chivundi ndi fungo lonunkha. Zoonadi Chauta adachita zazikulu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Ine ndidzachotsa ankhondo akumpoto kuti apite kutali ndi inu, kuwapirikitsira ku dziko lowuma ndi lachipululu, gulu lawo lakutsogolo ndidzalipirikitsira ku nyanja ya kummawa ndi gulu lawo lakumbuyo, ku nyanja ya kumadzulo. Ndipo mitembo yawo idzawola, fungo lake lidzamveka.” Zoonadi Yehova wachita zinthu zazikulu. |
Nati Hazaele, Koma nanga kapolo wanu ali chiyani, ndiye galu, kuti akachite chinthu chachikulu ichi? Nayankha Elisa, Yehova wandionetsa kuti udzakhala mfumu ya pa Aramu.
Ndipo Yehova anabweza mphepo yolimbatu ya kumadzulo, imene inapita nalo dzombe niliponya mu Nyanja Yofiira: silinatsale dzombe limodzi pakati pa malire onse a Ejipito.
Ophedwa aonso adzatayidwa kunja, ndipo kununkha kwa mitembo yao kudzamveka, ndipo mapiri adzasungunuka ndi mwazi wao.
Ndi mbali ya kum'mawa pakati pa Haurani, ndi Damasiko, ndi Giliyadi, ndi dziko la Israele, ndiwo Yordani; muyese kuyambira malire a kumpoto kufikira nyanja ya kum'mawa. Ndiyo mbali ya kum'mawa.
Ndinatumiza mliri pakati panu monga mu Ejipito; anyamata anu ndawapha ndi lupanga, ndi kutenga akavalo anu; ndipo ndinakweretsa kununkha kwa chigono chanu kufikitsa kumphuno kwanu; koma simunabwerere kudza kwa Ine, ati Yehova.
Ndipo kudzachitika tsiku lomwelo kuti madzi amoyo adzatuluka ku Yerusalemu; gawo lao lina kunka ku nyanja ya kum'mawa, ndi gawo lina kunka ku nyanja ya kumadzulo; adzatero nyengo ya dzinja ndi ya mwamvu.
Ndipo ndidzadzudzula zolusa chifukwa cha inu, kuti zisakuonongereni zipatso za nthaka yanu; ngakhale mpesa wanu sudzayoyoka zipatso zake, zosacha m'munda, ati Yehova wa makamu.
Pamalo ponse padzapondapo phazi lanu ndi panu, kuyambira chipululu ndi Lebanoni, kuyambira pamtsinjewo, mtsinje wa Yufurate, kufikira nyanja ya m'tsogolo, ndiwo malire anu.