Yoweli 1:20 - Buku Lopatulika Inde nyama zakuthengo zilira kwa Inu; pakuti mitsinje yamadzi yaphwa, ndi moto wapsereza mabusa a m'chipululu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Inde nyama zakuthengo zilira kwa Inu; pakuti mitsinje yamadzi yaphwa, ndi moto wapsereza mabusa a m'chipululu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nazonso nyama zakuthengo zikulira kwa Inu, chifukwa timitsinje tonse taphwa, ndipo moto wapsereza mabusa akuthengo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ngakhale nyama zakuthengo zikulirira Inu; timitsinje tonse taphwa ndipo moto wapsereza msipu wa kuthengo. |
Ndipo Ahabu anati kwa Obadiya, Kayendere dziko lonse ku zitsime zonse zamadzi, ndi ku mitsinje yonse, kapena tikapeza msipu ndi kusunga moyo wa akavalo ndi nyuru, zingafe nyama zonse.
Amkonzeratu khwangwala chakudya chake ndani, pamenepo ana ake afuulira kwa Mulungu, naulukauluka osowa chakudya?
Chifukwa cha nthaka yochita ming'alu, pakuti panalibe mvula padziko, olima ali ndi manyazi, afunda mitu yao.
Aneneri amene analipo kale ndisanakhale ine, nimusanakhale inu, ananenera maiko ambiri, ndi mafumu aakulu, za nkhondo, ndi za choipa, ndi za mliri.
Ha! Nyama ziusa moyo, magulu a ng'ombe azimidwa; pakuti zisowa podyera; magulu a nkhosa omwe atha.