Yoweli 1:16 - Buku Lopatulika Chakudya sichichotsedwa kodi pamaso pathu? Chimwemwe ndi chikondwerero pa nyumba ya Mulungu wathu? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chakudya sichichotsedwa kodi pamaso pathu? Chimwemwe ndi chikondwerero pa nyumba ya Mulungu wathu? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chakudya chathu chikutha ife tikuwona. Mulibenso chimwemwe ndi chisangalalo m'Nyumba ya Mulungu wathu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kodi chakudya chathu sichachotsedwa ife tikuona? Kodi mʼnyumba ya Mulungu wathu simulibe chimwemwe ndi chisangalalo? |
Kuti ndipite kufikira guwa la nsembe la Mulungu, kufikira Mulungu wa chimwemwe changa chenicheni, ndi kuti ndikuyamikeni ndi zeze, Mulungu, Mulungu wanga.
tsiku limenelo adzakweza mau ake, kuti, Sindine wochiritsa, chifukwa kuti m'nyumba mwanga mulibe chakudya kapena chovala; inu simudzandiyesa ine wolamulira anthu.
Mudzimangire chiguduli m'chuuno mwanu, nimulire, ansembe inu; bumani otumikira kuguwa la nsembe inu; lowani, gonani usiku wonse m'chiguduli, inu otumikira Mulungu wanga; pakuti nsembe yaufa ndi nsembe yothira zaletsedwera nyumba ya Mulungu wanu.