tsiku lako looka uzingapo mpanda, nuphukitsa mbeu zako m'mawa mwake; mulu wa masika udzaoneka tsiku lakulira ndi la chisoni chothetsa nzeru.
Yoweli 1:11 - Buku Lopatulika Gomani, akulima m'minda inu; lirani, akulima mpesa; chifukwa cha tirigu ndi barele; pakuti dzinthu za m'minda zatayika. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Gomani, akulima m'minda inu; lirani, akulima mpesa; chifukwa cha tirigu ndi barele; pakuti dzinthu za m'minda zatayika. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tayani mtima, inu alimi, lirani, inu olima mphesa, chifukwa tirigu ndi barele, ndi zonse zam'minda zalephera. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Khalani ndi nkhawa, inu alimi, lirani mofuwula inu alimi a mphesa; imvani chisoni chifukwa cha tirigu ndi barele, pakuti zokolola za mʼmunda zawonongeka. |
tsiku lako looka uzingapo mpanda, nuphukitsa mbeu zako m'mawa mwake; mulu wa masika udzaoneka tsiku lakulira ndi la chisoni chothetsa nzeru.
Yuda alira, ndipo zipata zake zilefuka, zikhala pansi zovekedwa ndi zakuda; mfuu wa Yerusalemu wakwera.
Muwathe ofesa ku Babiloni, ndi iwo amene agwira chisenga nyengo ya masika; chifukwa cha lupanga losautsa adzatembenukira yense kwa anthu ake, nadzathawira yense ku dziko lake.
Wanzeru ndani, kuti adziwe ichi? Ndani iye amene kamwa la Yehova lanena naye, kuti achilalikire? Chifukwa chake dziko litha ndi kupserera monga chipululu, kuti anthu asapitemo?
Chifukwa chake atero Yehova, Mulungu wa makamu, Ambuye, M'makwalala onse mudzakhala kulira, ndi m'miseu yonse adzati, Kalanga ine! Kalanga ine! Nadzaitana wakumunda adze kumaliro, ndi odziwa maliridwe a nthetemya alire.
ndipo chiyembekezo sichichititsa manyazi; chifukwa chikondi cha Mulungu chinatsanulidwa m'mitima mwathu mwa Mzimu Woyera, amene wapatsidwa kwa ife.