Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Yoswa 5:3 - Buku Lopatulika

Ndipo Yoswa anadzisemera mipeni yamiyala nadula ana a Israele pa Gibea-Naraloti.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo Yoswa anadzisemera mipeni yamiyala nadula ana a Israele pa Gibea-Naraloti.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Yoswa adasemadi mipeni yamiyalayo, naŵaumbala onsewo ku phiri lotchedwa “Koumbalira.”

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Choncho Yoswa anapanga mipeni ya miyala ndi kuchita mdulidwe Aisraeli ku Gibeyati Haaraloti.

Onani mutuwo



Yoswa 5:3
5 Mawu Ofanana  

Koma Zipora anatenga mpeni wamwala, nadula khungu la mwana wake, naliponya pa mapazi ake; nati, Pakuti iwe ndiwe mkwati wanga wamwazi. Ndipo Iye anamleka.


Pomwepo Yesu anati kwa ophunzira ake, Ngati munthu afuna kudza pambuyo panga, adzikane yekha, natenge mtanda wake, nanditsate Ine.


Nthawi imeneyo Yehova anati kwa Yoswa, Udzisemere mipeni yamiyala nudulenso ana a Israele kachiwiri.


Koma chifukwa chakuti Yoswa anawadula ndi ichi: anthu onse otuluka mu Ejipito, anthu aamuna, ndiwo amuna onse ankhondo, adafa m'chipululu panjira, atatuluka mu Ejipito.