Pamalo ponse padzapondapo phazi lanu ndi panu, kuyambira chipululu ndi Lebanoni, kuyambira pamtsinjewo, mtsinje wa Yufurate, kufikira nyanja ya m'tsogolo, ndiwo malire anu.
Yoswa 1:3 - Buku Lopatulika Pali ponse phazi lanu lidzapondapo ndinakupatsani, monga ndinanena ndi Mose. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pali ponse phazi lanu lidzapondapo ndinakupatsani, monga ndinanena ndi Mose. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Paliponse pamene muponde phazi lanu, ndakupatsani inu, monga momwe ndidalonjezera Mose. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Paliponse pamene phazi lanu liponde, ndikupatsani monga momwe ndinalonjezera Mose. |
Pamalo ponse padzapondapo phazi lanu ndi panu, kuyambira chipululu ndi Lebanoni, kuyambira pamtsinjewo, mtsinje wa Yufurate, kufikira nyanja ya m'tsogolo, ndiwo malire anu.
m'chiyembekezo cha moyo wosatha, umene Mulungu, wosanamayo, analonjeza zisanayambe nthawi zosayamba;
Kuyambira chipululu, ndi Lebanoni uyu, kufikira mtsinje waukulu mtsinje wa Yufurate, dziko lonse la Ahiti, ndi kufikira Nyanja Yaikulu ku malowero a dzuwa, ndiwo malire anu.
Ndipo Mose analumbira tsiku lomwelo ndi kuti, Zedi, dzikoli phazi lako lapondapo lidzakhala cholowa chako, ndi cha ana ako kosalekeza, chifukwa unatsata Yehova Mulungu wanga ndi mtima wonse.