Yohane 9:9 - Buku Lopatulika Ena ananena, kuti, Ndiyeyu; ena ananena, Iai, koma afanana naye. Iyeyu anati, Ndine amene. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ena ananena, kuti, Ndiyeyu; ena ananena, Iai, koma afanana naye. Iyeyu anati, Ndine amene. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ena adati, “Ndiye amene.” Ena nkumati, “Iyai, akungofanafana naye.” Koma mwiniwakeyo adati, “Ai ndithu, ndine amene.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ena ananena kuti anali yemweyo. Ena anati, “Ayi, sakuoneka ngati yemweyo.” Koma iye mwini ananenetsa kuti, “Munthuyo ndine.” |
Chifukwa chake anzake ndi iwo adamuona kale, kuti anali wopemphapempha, ananena, Kodi si uyu uja wokhala ndi kupemphapempha?