Yohane 9:6 - Buku Lopatulika Pamene ananena izi, analavula pansi, nakanda thope ndi malovuwo, napaka thopelo m'maso, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamene ananena izi, analavula pansi, nakanda thope ndi malovuwo, napaka thopelo m'maso, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Atanena zimenezi, Yesu adalavulira malovu pansi, nakanda thope ndi malovuwo. Kenaka adapaka thopelo m'maso mwa munthuyo, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Atanena izi, Iye anathira malovu pansi ndi kukanda dothi, napaka matopewo mʼmaso a munthuyo. |
Ndipo anampatula pa khamu la anthu pa yekha, nalonga zala zake m'makutu mwake, nalavula malovu, nakhudza lilime lake:
Ndipo anamgwira dzanja munthu wakhunguyo, natulukira naye kunja kwa mudzi; ndipo atamthira malovu m'maso mwake, naika manja pa iye, anamfunsa, Uona kanthu kodi?
Iyeyu anayankha, Munthuyo wotchedwa Yesu anakanda thope, napaka m'maso mwanga, nati, kwa ine, Muka ku Siloamu kasambe; chifukwa chake ndinachoka, ndipo m'mene ndinasamba ndinapenya.
ndikulangiza ugule kwa Ine golide woyengeka m'moto, kuti ukakhale wachuma, ndi zovala zoyera, kuti ukadziveke, ndi kuti manyazi a usiwa wako asaoneke; ndi mankhwala opaka m'maso mwako, kuti ukaone.