Yohane 9:30 - Buku Lopatulika Munthuyu anayankha nati kwa iwo, Pakuti chozizwa chili m'menemo, kuti inu simudziwa kumene achokera, ndipo ananditsegulira maso anga. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Munthuyu anayankha nati kwa iwo, Pakuti chozizwa chili m'menemo, kuti inu simudziwa kumene achokera, ndipo ananditsegulira maso anga. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Munthuyo adati, “Pakudabwitsatu mpamenepa: kuti inuyo simukudziŵa kumene Iye wachokera, komabe wandipenyetsa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Munthuyo anayankha kuti, “Tsopano izi ndi zodabwitsa! Inu simukudziwa kumene akuchokera, komabe iye watsekula maso anga. |
chifukwa chake, taonani, ndidzachitanso mwa anthu awa ntchito yodabwitsa, ngakhale ntchito yodabwitsa ndi yozizwitsa; ndipo nzeru ya anthu ao anzeru idzatha, ndi luntha la anthu ao ozindikira lidzabisika.
Ndipo tsiku limenelo gonthi adzamva mau a m'buku, ndi maso akhungu adzaona potuluka m'zoziya ndi mumdima.
akhungu alandira kuona kwao, ndi opunduka miyendo ayenda, akhate akonzedwa, ndi ogontha akumva, ndi akufa aukitsidwa, ndi kwa aumphawi ulalikidwa Uthenga Wabwino.
Yesu ananena kwa iwo, Kodi simunawerenge konse m'malembo, Mwala umene anaukana omanga nyumba womwewu unakhala mutu wa pangodya: Ichi chinachokera kwa Ambuye, ndipo chili chozizwitsa m'maso mwathu?
Ndipo anazizwa chifukwa cha kusakhulupirira kwao. Ndipo anayendayenda m'midzi yozungulirapo, naphunzitsa.
Ndipo anayankha, nati kwa iwo, Mukani, muuze Yohane zimene mwaziona, nimwazimva; anthu akhungu alandira kuona kwao, opunduka miyendo ayenda, akhate akonzedwa, ogontha akumva, akufa aukitsidwa, kwa aumphawi ulalikidwa Uthenga Wabwino.
Tidziwa kuti Mulungu samvera ochimwa. Koma ngati munthu aliyense akhala wopembedza Mulungu nachita chifuniro chake, amvera ameneyo.
Pakuti Mulungu amene anati, Kuunika kudzawala kutuluka mumdima, ndiye amene anawala m'mitima yathu kutipatsa chiwalitsiro cha chidziwitso cha ulemerero wa Mulungu pankhope pa Yesu Khristu.