Koma iyeyu anayankha iwo, Iye amene anandichiritsa, yemweyu anati kwa ine, Yalula mphasa yako, nuyende.
Yohane 9:25 - Buku Lopatulika Pamenepo iyeyu anayankha, Ngati ali wochimwa, sindidziwa; chinthu chimodzi ndichidziwa, pokhala ndinali wosaona, tsopano ndipenya. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamenepo iyeyu anayankha, Ngati ali wochimwa, sindidziwa; chinthu chimodzi ndichidziwa, pokhala ndinali wosaona, tsopano ndipenya. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Iye adati, “Zakuti Iye ngwochimwa, ine sindikudziŵa. Chinthu chimodzi chokha ndikudziŵa, kuti kale ndinali wosapenya, koma tsopano ndikupenya.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye anayankha kuti, “Zakuti Iye ndi wochimwa kapena ayi, ine sindikudziwa. Ine ndikudziwa chinthu chimodzi. Ndinali wosaona koma tsopano ndikuona!” |
Koma iyeyu anayankha iwo, Iye amene anandichiritsa, yemweyu anati kwa ine, Yalula mphasa yako, nuyende.
Pamenepo anamuitana kachiwiri munthuyo amene anali wosaona, nati kwa iye, Lemekeza Mulungu; tidziwa kuti munthuyo ali wochimwa.
Chifukwa chake anati kwa iye, Anakuchitira iwe chiyani? Anakutsegulira iwe maso bwanji?
Munthuyu anayankha nati kwa iwo, Pakuti chozizwa chili m'menemo, kuti inu simudziwa kumene achokera, ndipo ananditsegulira maso anga.
Iye amene amkhulupirira Mwana wa Mulungu ali nao umboni mwa iye; iye wosakhulupirira Mulungu anamuyesa Iye wonama; chifukwa sanakhulupirire umboni wa Mulungu anauchita wa Mwana wake.