Ndipo mkazi, anali ndi nthenda yachidwalire zaka khumi ndi ziwiri, amene adasudzula asing'anga za moyo wake zonse, ndipo sanathe kuchiritsidwa ndi mmodzi yense,
Yohane 9:21 - Buku Lopatulika koma sitidziwa uno apenyera tsopano; kapena sitimdziwa mene anamtsegulira pamaso pake; mumfunse iye; ali wamsinkhu; adzalankhula mwini za iye yekha. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 koma sitidziwa uno apenyera tsopano; kapena sitimdziwa mene anamtsegulira pamaso pake; mumfunse iye; ali wamsinkhu; adzalankhula mwini za iye yekha. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma kuti tsopano akupenya, sitikudziŵa m'mene zachitikira. Zoti wamupenyetsa ndani kaya, ife sitikudziŵanso. Mufunseni mwiniwakeyu, ngwamkulu, afotokoze yekha.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma sitidziwa zimene zachitika kuti tsopano azipenya. Amenenso wamupenyetsa sitikumudziwa. Mufunseni ndi wamkulu; iye adziyankhira yekha.” |
Ndipo mkazi, anali ndi nthenda yachidwalire zaka khumi ndi ziwiri, amene adasudzula asing'anga za moyo wake zonse, ndipo sanathe kuchiritsidwa ndi mmodzi yense,
Koma panali munthu wina apo, ali m'kudwala kwake zaka makumi atatu kudza zisanu ndi zitatu.
Ndipo apenya bwanji tsopano? Atate wake ndi amake anayankha nati, Tidziwa kuti uyu ndi mwana wathu, ndi kuti anabadwa wosaona;
Izi ananena atate wake ndi amake, chifukwa anaopa Ayuda; pakuti Ayuda adapangana kale, kuti ngati munthu aliyense adzamvomereza Iye kuti ndiye Khristu, akhale woletsedwa m'sunagoge.
Ndipo anapeza kumeneko munthu dzina lake Eneya, amene anagonera pamphasa zaka zisanu ndi zitatu; amene anagwidwa manjenje.