Ndipo anatuluka Loti nanena nao akamwini ake amene amayenera kukwatira ana ake aakazi, nati, Taukani, tulukani m'malo muno; popeza Yehova adzaononga mzindawu; koma akamwini ake anamyesa wongoseka.
Yohane 9:18 - Buku Lopatulika Chifukwa chake Ayuda sanakhulupirire za iye, kuti anali wosaona, napenya, kufikira kumene adaitana atate wake ndi amake a iye wopenya; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chifukwa chake Ayuda sanakhulupirire za iye, kuti anali wosaona, napenya, kufikira kumene adaitana atate wake ndi amake a iye wopenya; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma akulu a Ayudawo sadakhulupirire kuti munthuyo kale sankapenya ndipo tsopano akupenya, mpaka adaitanitsa makolo ake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ayuda sanakhulupirirebe kuti iye anali wosaona ndi kuti anayamba kuona kufikira atayitana makolo ake. |
Ndipo anatuluka Loti nanena nao akamwini ake amene amayenera kukwatira ana ake aakazi, nati, Taukani, tulukani m'malo muno; popeza Yehova adzaononga mzindawu; koma akamwini ake anamyesa wongoseka.
Yehova, dzanja lanu litukulidwa, koma iwo saona; koma iwo adzaona changu chanu cha kwa anthu, nadzakhala ndi manyazi; inde moto udzamaliza adani anu.
Koma anati kwa iye, Ngati samvera Mose ndi aneneri, sadzakopeka mtima ngakhale wina akauka kwa akufa.
Ndipo umene ndiwo umboni wa Yohane, pamene Ayuda anatuma kwa iye ansembe ndi Alevi a ku Yerusalemu akamfunse iye, Ndiwe yani?
Mungathe inu bwanji kukhulupirira, popeza mulandira ulemu wina kwa mnzake ndipo ulemu wakuchokera kwa Mulungu yekha simuufuna?
nawafunsa iwo, nanena, Kodi uyu ndi mwana wanu, amene inu munena kuti anabadwa wosaona?
Izi ananena atate wake ndi amake, chifukwa anaopa Ayuda; pakuti Ayuda adapangana kale, kuti ngati munthu aliyense adzamvomereza Iye kuti ndiye Khristu, akhale woletsedwa m'sunagoge.
Chifukwa chake tichite changu cha kulowa mpumulowo, kuti wina angagwe m'chitsanzo chomwe cha kusamvera.