Koma ansembe aakulu ndi Afarisi adalamula kuti, munthu wina akadziwa pokhala Iye, aulule, kuti akamgwire Iye.
Yohane 9:13 - Buku Lopatulika Anapita naye amene anali wosaona kale kwa Afarisi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Anapita naye amene anali wosaona kale kwa Afarisi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono munthu uja kale sankapenyayu adapita naye kwa Afarisi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iwo anabwera naye munthu amene poyamba anali wosaona kwa Afarisi. |
Koma ansembe aakulu ndi Afarisi adalamula kuti, munthu wina akadziwa pokhala Iye, aulule, kuti akamgwire Iye.
Chifukwa chake Afarisi ananena wina ndi mnzake, Muona kuti simupindula kanthu konse; onani dziko litsata pambuyo pake pa Iye.
Kungakhale kotero, ambiri a mwa akulu anakhulupirira Iye; koma chifukwa cha Afarisi sanavomereze, kuti angaletsedwe m'sunagoge,