Ndipo anamfunsa Baruki, kuti, Utifotokozeretu, Unalemba bwanji mau awa onse ponena iye?
Yohane 9:11 - Buku Lopatulika Iyeyu anayankha, Munthuyo wotchedwa Yesu anakanda thope, napaka m'maso mwanga, nati, kwa ine, Muka ku Siloamu kasambe; chifukwa chake ndinachoka, ndipo m'mene ndinasamba ndinapenya. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Iyeyu anayankha, Munthuyo wotchedwa Yesu anakanda thope, napaka m'maso mwanga, nati, kwa ine, Muka ku Siloamu kasambe; chifukwa chake ndinachoka, ndipo m'mene ndinasamba ndinapenya. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Iyeyo adati, “Munthu uja amati Yesuyu anakanda thope nalipaka m'maso mwangamu. Kenaka anandiwuza kuti, ‘Pita, ukasambe ku Siloamu. Ndinapitadi, ndipo nditasamba, ndayamba kupenya.’ ” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye anayankha kuti, “Munthu wina wotchedwa Yesu anakanda dothi ndi kupaka mʼmaso anga. Iye anandiwuza kuti ndipite ku Siloamu ndi kukasamba. Choncho ndinapita kukasamba, ndipo ndikuona.” |
Ndipo anamfunsa Baruki, kuti, Utifotokozeretu, Unalemba bwanji mau awa onse ponena iye?
Kapena iwo aja khumi ndi asanu ndi atatu, amene nsanja yaitali ya mu Siloamu inawagwera, ndi kuwapha; kodi muyesa kuti iwo anali olakwa koposa anthu onse akukhala m'Yerusalemu?
Iye anayankha iwo, Ndinakuuzani kale, ndipo simunamve; mufuna kumvanso bwanji? Kodi inunso mufuna kukhala ophunzira ake?