Pakuti kwa ife mwana wakhanda wabadwa, kwa ife mwana wamwamuna wapatsidwa; ndipo ulamuliro udzakhala pa phewa lake, ndipo adzamutcha dzina lake Wodabwitsa, Wauphungu, Mulungu wamphamvu, Atate Wosatha, Kalonga wa mtendere.
Yohane 8:53 - Buku Lopatulika Kodi Inu ndinu wamkulu ndi atate wathu Abrahamu, amene anamwalira? Ndipo aneneri anamwalira: mudziyesera nokha muli yani? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Kodi Inu ndinu wamkulu ndi atate wathu Abrahamu, amene anamwalira? Ndipo aneneri anamwalira: mudziyesera nokha muli yani? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Monga Iweyo nkupambana atate athu Abrahamu amene adamwalira? Anenerinso adamwalira. Kodi umadziyesa yani?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kodi ndinu wa mkulu kuposa abambo athu Abrahamu? Iye anafa, ndiponso aneneri onse. Inu mukuganiza kuti ndinu yani?” |
Pakuti kwa ife mwana wakhanda wabadwa, kwa ife mwana wamwamuna wapatsidwa; ndipo ulamuliro udzakhala pa phewa lake, ndipo adzamutcha dzina lake Wodabwitsa, Wauphungu, Mulungu wamphamvu, Atate Wosatha, Kalonga wa mtendere.
ndipo musamayesa kunena mwa inu nokha, Atate wathu tili naye Abrahamu; pakuti ndinena kwa inu kuti mwa miyala iyi Mulungu akhoza kuukitsira Abrahamu ana.
Ayuda anamyankha Iye, Chifukwa cha ntchito yabwino sitikuponyani miyala, koma chifukwa cha mwano; ndi kuti Inu, muli munthu, mudziyesera nokha Mulungu.
Pamenepo khamulo linayankha Iye, Tidamva ife m'chilamulo kuti Khristu akhala kunthawi yonse; ndipo Inu munena bwanji, kuti Mwana wa Munthu ayenera kukwezedwa? Mwana wa Munthu amene ndani?
Ayuda anamyankha iye, Tili nacho chilamulo ife, ndipo monga mwa chilamulocho ayenera kufa, chifukwa anadziyesera Mwana wa Mulungu.
Kodi muli wamkulu ndi atate wathu Yakobo amene anatipatsa ife chitsimechi, namwamo iye yekha, ndi ana ake, ndi zoweta zake?
Chifukwa cha ichi Ayuda anaonjeza kufuna kumupha, si chifukwa cha kuswa tsiku la Sabata kokha, komatu amatchanso Mulungu Atate wake wa Iye yekha; nadziyesera wolingana ndi Mulungu.
Yesu anati kwa iwo, Indetu, indetu, ndinena kwa inu, asanayambe kukhala Abrahamu ndipo Ine ndilipo.
a iwo ali makolo, ndi kwa iwo anachokera Khristu, monga mwa thupi, ndiye Mulungu wa pamwamba pa zonse wolemekezeka kunthawi zonse. Amen.