Yohane 8:40 - Buku Lopatulika Koma tsopano mufuna kundipha Ine, ndine munthu amene ndinalankhula ndi inu choonadi, chimene ndinamva kwa Mulungu; ichi Abrahamu sanachite. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma tsopano mufuna kundipha Ine, ndine munthu amene ndinalankhula ndi inu choonadi, chimene ndinamva kwa Mulungu; ichi Abrahamu sanachite. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma tsopano mukufuna kundipha Ine, amene ndakuuzani zoona zimene ndidamva kwa Mulungu. Abrahamu sadachite zotere. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma mmene zililimu, inu mwatsimikiza kundipha Ine, munthu amene ndinakuwuzani choonadi chimene Ine ndinachimva kuchokera kwa Mulungu. Abrahamu sanachite zinthu zoterezi. |
Ndipo zitapita izi Yesu anayendayenda mu Galileya; pakuti sanafune kuyendayenda mu Yudeya, chifukwa Ayuda anafuna kumupha Iye.
Ndili nazo zambiri zakulankhula ndi zakuweruza za inu; koma wondituma Ine ali woona; ndipo zimene ndazimva kwa Iye, zomwezo ndilankhula kwa dziko lapansi.
ndiponso kholo la mdulidwe wa iwo amene siali a mdulidwe okha, koma wa iwo amene atsata mayendedwe a chikhulupiriro chija cha kholo lathu Abrahamu, chimene iye anali nacho asanadulidwe.
Komatu monga pompaja iye wobadwa monga mwa thupi anazunza wobadwa monga mwa Mzimu, momwemonso tsopano.
Ndipo chinjoka chinakwiya ndi mkazi, ndipo chinachoka kunka kuchita nkhondo ndi otsala a mbeu yake, amene asunga malamulo a Mulungu, nakhala nao umboni wa Yesu.
Ndipo mchira wake uguza limodzi la magawo atatu a nyenyezi zam'mwamba, nuziponya padziko. Ndipo chinjoka chinaimirira pamaso pa mkazi akuti abale, kuti, akabala icho chikalikwire mwana wake.