Yohane 8:30 - Buku Lopatulika Pakulankhula Iye zimenezi ambiri anakhulupirira Iye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakulankhula Iye zimenezi ambiri anakhulupirira Iye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamene Yesu ankalankhula zimenezi, anthu ambiri adamkhulupirira. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamene Iye ankayankhula zimenezi, ambiri anamukhulupirira. |
Chifukwa chake ambiri a mwa Ayuda amene anadza kwa Maria, m'mene anaona chimene anachita, anakhulupirira Iye.
Koma pamene anali mu Yerusalemu pa Paska pachikondwerero, ambiri anakhulupirira dzina lake, pakuona zizindikiro zake zimene anachitazi.
Chifukwa chake, anthu, poona chizindikiro chimene anachita, ananena, kuti, Ameneyo ndiye mneneri ndithu wakudzayo m'dziko lapansi.
Koma ambiri a m'khamu la anthu anakhulupirira Iye; ndipo ananena, Pamene Khristu akadza kodi adzachita zizindikiro zambiri zoposa zimene adazichita ameneyo?