Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Yohane 8:25 - Buku Lopatulika

Pamenepo ananena kwa Iye, Ndinu yani? Yesu anati kwa iwo, Chimene chomwe ndidalankhulanso ndi inu kuyambira pachiyambi.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Pamenepo ananena kwa Iye, Ndinu yani? Yesu anati kwa iwo, Chimene chomwe ndidalankhulanso ndi inu kuyambira pachiyambi.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Apo iwo adamufunsa kuti, “Iweyo ndiwe yani?” Yesu adati, “Nchomwe ndakhala ndikukuuzani chiyambire ndithu.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Iwo anafunsa kuti, “Ndinu ndani?” Yesu anayankha kuti, “Monga Ine ndakhala ndikunena nthawi yonseyi,

Onani mutuwo



Yohane 8:25
9 Mawu Ofanana  

nanena, Ngati uli Khristu, utiuze. Ndipo anati kwa iwo, Ndikakuuzani, simudzavomereza;


Ndipo umene ndiwo umboni wa Yohane, pamene Ayuda anatuma kwa iye ansembe ndi Alevi a ku Yerusalemu akamfunse iye, Ndiwe yani?


Chifukwa chake anati kwa iye, Ndiwe yani? Kuti tibwezere mau kwa iwo anatituma ife. Unena chiyani za iwe wekha?


Pamenepo Ayuda anamzungulira Iye, nanena ndi Iye, Kufikira liti musinkhitsasinkhitsa moyo wathu? Ngati Inu ndinu Khristu, tiuzeni momveka.


Ndipo analowanso ku Pretorio, nanena kwa Yesu, Muchoka kuti? Koma Yesu sanamyankhe kanthu.


Pamenepo Yesu analankhulanso nao, nanena, Ine ndine kuunika kwa dziko lapansi; iye wonditsata Ine sadzayenda mumdima, koma adzakhala nako kuunika kwa moyo.


Chifukwa chake ndinati kwa inu, kuti mudzafa m'machimo kwa inu, kuti mudzafa m'machimo anu, pakuti ngati simukhulupirira kuti Ine ndine, mudzafa m'machimo anu.


Ndili nazo zambiri zakulankhula ndi zakuweruza za inu; koma wondituma Ine ali woona; ndipo zimene ndazimva kwa Iye, zomwezo ndilankhula kwa dziko lapansi.