Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Yohane 8:23 - Buku Lopatulika

Ndipo ananena nao, Inu ndinu ochokera pansi; Ine ndine wochokera Kumwamba; inu ndinu a dziko lino lapansi; sindili Ine wa dziko lino lapansi.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo ananena nao, Inu ndinu ochokera pansi; Ine ndine wochokera Kumwamba; inu ndinu a dziko lino lapansi; sindili Ine wa dziko lino lapansi.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Yesu adaŵauza kuti, “Inu ndinu ochokera pansi pano, Ine ndine wochokera Kumwamba. Inu ndinu a dziko lino lapansi, Ine sindine wa dziko lino lapansi ai.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Koma Iye anapitiriza kuti, “Inu ndi ochokera pansi pano. Ine ndine wochokera kumwamba. Inu ndinu anthu a dziko la pansi. Ine sindine wa dziko lapansi lino.

Onani mutuwo



Yohane 8:23
15 Mawu Ofanana  

Za machitidwe a anthu, ndachenjera ndi mau a milomo yanu ndingalowe njira za woononga.


Ndipo Mau anasandulika thupi, nakhazikika pakati pa ife, ndipo tinaona ulemerero wake, ulemerero wonga wa wobadwa yekha wa Atate, wodzala ndi chisomo ndi choonadi.


Ine ndawapatsa iwo mau anu; ndipo dziko lapansi, linadana nao, chifukwa sakhala a dziko lapansi, monga Ine sindikhala wa dziko lapansi.


Siali a dziko lapansi monga Ine sindili wa dziko lapansi.


Ndipo kulibe munthu anakwera Kumwamba, koma Iye wotsikayo kuchokera Kumwamba, ndiye Mwana wa Munthu, wokhala mu Mwambayo.


Iye wochokera Kumwamba ali woposa onse; iye amene ali wa dziko lapansi ali wa dziko lapansi, nalankhula za dziko lapansi: Iye wochokera Kumwamba ali woposa onse.


Akazi achigololo inu, kodi simudziwa kuti ubwenzi wa dziko lapansi uli udani ndi Mulungu? Potero, iye amene afuna kukhala bwenzi la dziko lapansi adziika mdani wa Mulungu.