Yohane 8:22 - Buku Lopatulika Chifukwa chake Ayuda anenana, Kodi adzadzipha yekha, pakuti ananena, Kumene ndimukako Ine, simudziwa inu kudza? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chifukwa chake Ayuda anenana, Kodi adzadzipha yekha, pakuti ananena, Kumene ndimukako Ine, simudziwa inu kudza? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Apo Ayuda adati, “Kodi kapena akufuna kukadzipha, umo akunena kuti, ‘Kumene ndikupita Ine, inu simungathe kufikako?’ ” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Izi zinachititsa Ayuda kufunsa kuti, “Kodi adzadzipha yekha? Kodi ndicho chifukwa chake akuti, ‘Kumene ndikupita, inu simungabwereko?’ ” |
Koma ine ndine nyongolotsi, si munthu ai, chotonza cha anthu, ndi wonyozedwa ndi anthu.
Ikhale yosalankhula milomo ya mabodza, imene imalankhula mwachipongwe pa olungama mtima, ndi kudzikuza ndi kunyoza.
Ndipo umene ndiwo umboni wa Yohane, pamene Ayuda anatuma kwa iye ansembe ndi Alevi a ku Yerusalemu akamfunse iye, Ndiwe yani?
Chifukwa chake Ayuda anati mwa iwo okha, Adzanka kuti uyu kuti ife sitikampeza Iye? Kodi adzamuka kwa Agriki obalalikawo, ndi kuphunzitsa Agriki?
Ayuda anayankha nati kwa Iye, Kodi sitinenetsa kuti Inu ndinu Msamariya, ndipo muli ndi chiwanda?
Ayuda anati kwa Iye, Tsopano tazindikira kuti muli ndi chiwanda. Abrahamu anamwalira, ndi aneneri; ndipo Inu munena, Munthu akasunga mau anga, sadzalawa imfa kunthawi yonse.
Pakuti talingirirani Iye amene adapirira ndi ochimwa otsutsana naye kotere, kuti mungaleme ndi kukomoka m'moyo mwanu.