ndipo muike anthu awiri, anthu oipa, pamaso pake, kuti amchitire umboni, ndi kuti, Watemberera Mulungu ndi mfumu; nimumtulutse ndi kumponya miyala kumupha.
Yohane 8:17 - Buku Lopatulika Inde kudalembedwa m'chilamulo chanu kuti umboni wa anthu awiri uli woona. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Inde kudalembedwa m'chilamulo chanu kuti umboni wa anthu awiri uli woona. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndipo m'Malamulo anu mudalembedwa kuti umboni wa anthu aŵiri ngwokwanira. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mʼmalamulo anu munalembedwa kuti umboni wa anthu awiri ndi wovomerezeka. |
ndipo muike anthu awiri, anthu oipa, pamaso pake, kuti amchitire umboni, ndi kuti, Watemberera Mulungu ndi mfumu; nimumtulutse ndi kumponya miyala kumupha.
Aliyense wakantha munthu, wakupha munthuyo aziphedwa pakamwa pa mboni; koma mboni ya munthu mmodzi isafikire kuti munthu afe.
Koma ngati samvera, onjeza kutenga ndi iwe wina mmodzi kapena awiri, kuti atsimikizidwe mau onse pakamwa pa mboni ziwiri kapena zitatu.
Koma chitero, kuti mau olembedwa m'chilamulo chao akwaniridwe, kuti, Anandida Ine kopanda chifukwa.
Nthawi yachitatu iyi ndilinkudza kwa inu. Pakamwa pa mboni ziwiri kapena zitatu maneno onse adzakhazikika.
Momwemo chilamulo chidakhala namkungwi wathu wakutifikitsa kwa Khristu, kuti tikayesedwe olungama ndi chikhulupiriro.
Pakamwa pa mboni ziwiri kapena zitatu amuphe iye amene akuti afe; asamuphe pakamwa pa mboni imodzi.
Mboni imodzi isamaukira munthu pa mphulupulu iliyonse, kapena tchimo lililonse adalichimwa; pakamwa pa mboni ziwiri, kapena pakamwa pa mboni zitatu mlandu utsimikizike.
Munthu wopeputsa chilamulo cha Mose angofa opanda chifundo pa mboni ziwiri kapena zitatu:
Ngati tilandira umboni wa anthu, umboni wa Mulungu uposa; chifukwa umboni wa Mulungu ndi uwu, kuti anachita umboni za Mwana wake.
Ndipo ndidzalamulira mboni zanga ziwiri, ndipo zidzanenera masiku chikwi chimodzi ndi mazana awiri amphambu makumi asanu ndi limodzi, zovala chiguduli.