Yohane 8:15 - Buku Lopatulika Inu muweruza monga mwa thupi; Ine sindiweruza munthu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Inu muweruza monga mwa thupi; Ine sindiweruza munthu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Inu mumaweruza potsata maganizo a anthu chabe. Ine sindiweruza munthu aliyense. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Inu mumaweruza potsata maganizo a anthu chabe. Ine sindiweruza munthu wina aliyense. |
Kodi akavalo adzathamanga pathanthwe? Kodi adzalimako ndi ng'ombe pakuti mwasanduliza chiweruzo chikhale ndulu, ndi chipatso cha chilungamo chikhale chivumulo;
Pakuti chilamulo chalekeka, ndi chiweruzo sichitulukira konse; popeza woipa azinga wolungama, chifukwa chake chiweruzo chituluka chopindika.
Koma anati kwa iye, Munthu iwe, ndani anandiika Ine ndikhale woweruza, kapena wakugawira inu?
Ndipo ngati wina akumva mau anga, ndi kusawasunga, Ine sindimweruza; pakuti sindinadze kudzaweruza dziko lapansi, koma kuti ndipulumutse dziko lapansi.
Yesu anayankha, Ufumu wanga suli wa dziko lino lapansi; ufumu wanga ukadakhala wa dziko lino lapansi, anyamata anga akadalimbika nkhondo, kuti ndisaperekedwe kwa Ayuda; koma tsopano ufumu wanga suli wochokera konkuno.
Pakuti Mulungu sanatume Mwana wake kudziko lapansi, kuti akaweruze dziko lapansi, koma kuti dziko lapansi likapulumutsidwe ndi Iye.
Koma iye anati, Palibe, Ambuye. Ndipo Yesu anati, Inenso sindikutsutsa iwe; pita; kuyambira tsopano usachimwenso.
Chifukwa chake uli wopanda mau owiringula, munthu iwe, amene uli yense wakuweruza; pakuti m'mene uweruza wina, momwemo udzitsutsa iwe wekha, pakuti iwe wakuweruza, umachita zomwezo.
Kotero kuti ife sitidziwanso munthu tsopano monga mwa thupi; ndipo ngati tazindikira Khristu monga mwa thupi, koma tsopano sitimzindikiranso motero.
Koma Yehova ananena ndi Samuele, Usayang'ane nkhope yake, kapena kutalika kwa msinkhu wake, popeza Ine ndinamkana iye; pakuti Yehova saona monga aona munthu; pakuti munthu ayang'ana chooneka ndi maso, koma Yehova ayang'ana mumtima.