Pakuti pali wina kodi anati kwa Mulungu, ndasenza kulanga kwanu, ndingakhale sindinalakwe?
Yohane 8:11 - Buku Lopatulika Koma iye anati, Palibe, Ambuye. Ndipo Yesu anati, Inenso sindikutsutsa iwe; pita; kuyambira tsopano usachimwenso. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma iye anati, Palibe, Ambuye. Ndipo Yesu anati, Inenso sindikutsutsa iwe; pita; kuyambira tsopano usachimwenso. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Maiyo adati, “Inde Ambuye, palibe.” Tsono Yesu adamuuza kuti, “Inenso sindikukuzengani mlandu. Pitani koma kuyambira tsopano musakachimwenso.”] Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye anati, “Ambuye, palibe ndi mmodzi yemwe.” “Inenso sindikukutsutsa iwe. Pita kuyambira tsopano usakachimwenso.” |
Pakuti pali wina kodi anati kwa Mulungu, ndasenza kulanga kwanu, ndingakhale sindinalakwe?
Ndinena kwa inu, Iaitu; koma ngati inu simutembenuka mtima, mudzaonongeka nonse momwemo.
Ndinena kwa inu, Iaitu; koma ngati simutembenuka mtima, mudzaonongeka nonse chimodzimodzi.
Chomwecho, ndinena kwa inu, kuli chimwemwe pamaso pa angelo a Mulungu chifukwa cha munthu wochimwa mmodzi amene atembenuka mtima.
Koma kudayenera kuti tisangalale ndi kukondwerera: chifukwa mng'ono wako uyu anali wakufa ndipo ali ndi moyo; anatayika, ndipo wapezeka.
Ndinena kwa inu, kotero kudzakhala chimwemwe Kumwamba chifukwa cha wochimwa mmodzi wotembenuka mtima, koposa anthu olungama makumi asanu ndi anai mphambu asanu ndi anai, amene alibe kusowa kutembenuka mtima.
Yesu anayankha, Ufumu wanga suli wa dziko lino lapansi; ufumu wanga ukadakhala wa dziko lino lapansi, anyamata anga akadalimbika nkhondo, kuti ndisaperekedwe kwa Ayuda; koma tsopano ufumu wanga suli wochokera konkuno.
Pakuti Mulungu sanatume Mwana wake kudziko lapansi, kuti akaweruze dziko lapansi, koma kuti dziko lapansi likapulumutsidwe ndi Iye.
Zitapita izi Yesu anampeza mu Kachisi, nati kwa iye, Taona, wachiritsidwa; usachimwenso, kuti chingakugwere choipa choposa.
Kapena upeputsa kodi kulemera kwa ubwino wake, ndi chilekerero ndi chipiriro chake, wosadziwa kuti ubwino wa Mulungu ukubwezera kuti ulape?
Pakuti nditani nao akunja kukaweruza iwo? Kodi amene ali m'katimo simuwaweruze ndi inu,
Mudziikire oweruza ndi akapitao m'midzi yanu yonse imene Yehova Mulungu wanu akupatsani, monga mwa mafuko anu; ndipo aweruze anthu ndi chiweruzo cholungama.
nimufike kwa ansembe, Alevi, ndi kwa woweruza wa m'masiku awo; nimufunsire; ndipo adzakufotokozerani maweruzidwe ake.
Ndipo yesani kulekerera kwa Ambuye wathu chipulumutso; monganso mbale wathu wokondedwa Paulo, monga mwa nzeru zopatsidwa kwa iye, anakulemberani;