Koma pamene anakhalakhala alikumfunsabe Iye, anaweramuka, nati kwa iwo, Amene mwa inu ali wopanda tchimo, ayambe kumponya mwala.
Yohane 8:10 - Buku Lopatulika Koma Yesu pamene adaweramuka, anati kwa iye, Mkazi iwe, ali kuti ajawa? Palibe munthu anakutsutsa kodi? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma Yesu pamene adaweramuka, anati kwa iye, Mkazi iwe, ali kuti ajawa? Palibe munthu anakutsutsa kodi? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kenaka Yesu adaŵeramuka namufunsa kuti, “Kodi mai, ali kuti anthu aja? Kodi palibe ndi mmodzi yemwe amene wakuzengani mlandu?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yesu anaweramuka ndipo anamufunsa iye kuti, “Akuluakulu aja ali kuti? Kodi palibe amene wakutsutsa?” |
Koma pamene anakhalakhala alikumfunsabe Iye, anaweramuka, nati kwa iwo, Amene mwa inu ali wopanda tchimo, ayambe kumponya mwala.
Koma iwo, m'mene anatulukamo amodziamodzi, kuyambira akulu, kufikira otsiriza; ndipo Yesu anatsala yekha, ndi mkazi, alikuima pakati.