Ndipo anati iwo, Baima; natinso, Uyu anadza kuno kukhala ngati mlendo, ndipo afuna kutilamulira; tsopano tidzakuchitira iwe koipa koposa iwo. Ndipo iwo anamkakamiza munthuyo Loti ndithu, nayandikira kuti aswe chitseko.
Yohane 7:52 - Buku Lopatulika Anayankha nati kwa iye, Kodi iwenso uli wotuluka mu Galileya? Santhula, nuone kuti mu Galileya sanauke mneneri. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Anayankha nati kwa iye, Kodi iwenso uli wotuluka m'Galileya? Santhula, nuone kuti m'Galileya sanauke mneneri. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Iwo adati, “Kani iwenso ndiwe wa ku Galileya? Kafunefune m'Malembo ndipo udzaona kuti palibe mneneri wochokera ku Galileya.” [ Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iwo anayankha kuti, “Kodi ndiwenso wochokera ku Galileya? Tayangʼananso, ndipo udzapeza kuti mneneri sachokera ku Galileya.” |
Ndipo anati iwo, Baima; natinso, Uyu anadza kuno kukhala ngati mlendo, ndipo afuna kutilamulira; tsopano tidzakuchitira iwe koipa koposa iwo. Ndipo iwo anamkakamiza munthuyo Loti ndithu, nayandikira kuti aswe chitseko.
Pamenepo Zedekiya mwana wa Kenana anasendera, napanda Mikaya patsaya, nati, Mzimu wa Yehova wandichokera bwanji, kulankhula ndi iwe?
Koma anati, Wakuika iwe ndani ukhale mkulu ndi woweruza wathu? Kuteroku ukuti undiphe, monga unamupha Mwejipito? Ndipo Mose anachita mantha, nanena, Ndithu chinthuchi chadziwika.
Natanaele anati kwa iye, Ku Nazarete nkutha kuchokera kanthu kabwino kodi? Filipo ananena naye, Tiye ukaone.
Musanthula m'malembo, popeza muyesa kuti momwemo muli nao moyo wosatha; ndipo akundichitira Ine umboni ndi iwo omwewo;
Ena ananena, Uyu ndi Khristu. Koma ena ananena, Kodi Khristu adza kutuluka mu Galileya?
Anayankha nati kwa iye, Wabadwa iwe konse m'zoipa, ndipo iwe utiphunzitse ife kodi? Ndipo anamtaya kunja.