Yohane 7:47 - Buku Lopatulika Pamenepo Afarisi anayankha iwo, Kodi mwasokeretsedwa inunso? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamenepo Afarisi anayankha iwo, Kodi mwasokeretsedwa inunso? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Apo Afarisi adati, “Kani inunso wakunyengani? Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Afarisi anawadzudzula nati, “Kodi mukutanthauza kuti Iye anakunamizani inunso?” |
mpaka ndifika ndi kumuka nanu ku dziko lakunga dziko lanu, dziko la tirigu ndi vinyo, dziko la mkate ndi minda yampesa, dziko la azitona ndi la uchi; kuti mukhale ndi moyo osafai; nimusamvere Hezekiya akakukopani, ndi kuti, Yehova adzatilanditsa.
Ndipo tsono, asakunyengeni Hezekiya, ndi kukukopani motero, musamkhulupirira; pakuti palibe Mulungu wa mtundu uliwonse wa anthu, kapena ufumu uliwonse, unakhoza kulanditsa anthu ake m'dzanja mwanga; ndipo kodi Mulungu wanu adzakulanditsani inu m'dzanja langa?
Ndipo Iye anayankha, nati kwa iwo, Inunso mulumphiranji lamulo la Mulungu chifukwa cha miyambo yanu?
nanena, Mfumu, takumbukira ife kuti wonyenga uja anati, pamene anali ndi moyo, Ndidzauka pofika masiku atatu.
Ndipo kunali kung'ung'udza kwambiri za Iye m'makamu a anthu; ena ananena, kuti, Ali wabwino; koma ena ananena, Iai, koma asocheretsa khamu la anthuwo.
mwa ulemerero, mwa mnyozo, mwa mbiri yoipa ndi mbiri yabwino; monga osocheretsa, angakhale ali oona;