Yohane 7:44 - Buku Lopatulika Koma ena mwa iwo anafuna kumgwira Iye; koma palibe munthu anamgwira kumanja. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma ena mwa iwo anafuna kumgwira Iye; koma palibe munthu anamgwira kumanja. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ena ankafuna kumgwira, koma panalibe amene adamkhudza. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ena anafuna kumugwira Iye, koma palibe amene anayika dzanja pa Iye. |
Pamenepo anafuna kumgwira Iye; koma palibe wina anamgwira kumanja, chifukwa nthawi yake siinafike.
Mau awa analankhula m'nyumba yosungiramo chuma cha Mulungu pophunzitsa mu Kachisi; ndipo palibe munthu anamgwira Iye, pakuti nthawi yake siinafike.
chifukwa Ine ndili pamodzi ndi iwe, ndipo palibe munthu adzautsana ndi iwe kuti akuipse; chifukwa ndili nao anthu ambiri m'mzinda muno.
Ndipo usiku wake Ambuye anaimirira pa iye, nati, Limbika mtima; pakuti monga wandichitira umboni ku Yerusalemu, koteronso uyenera kundichitira umboni ku Roma.