Pakuti ndinadza kusiyanitsa munthu ndi atate wake, ndi mwana wamkazi ndi amake, ndi mkazi wokwatiwa ndi mpongozi wake:
Yohane 7:43 - Buku Lopatulika Kudakhala tsono kusiyana m'khamulo chifukwa cha Iye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Kudakhala tsono kusiyana m'khamulo chifukwa cha Iye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Choncho khamu la anthu lidagaŵikana chifukwa cha Iye. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kotero anthu anagawikana chifukwa cha Yesu. |
Pakuti ndinadza kusiyanitsa munthu ndi atate wake, ndi mwana wamkazi ndi amake, ndi mkazi wokwatiwa ndi mpongozi wake:
Kodi muyesa kuti ndinadzera kudzapatsa mtendere padziko lapansi? Ndinena kwa inu, Iaitu, komatu kutsutsana;
Ndipo kunali kung'ung'udza kwambiri za Iye m'makamu a anthu; ena ananena, kuti, Ali wabwino; koma ena ananena, Iai, koma asocheretsa khamu la anthuwo.
Ena pamenepo mwa Afarisi ananena, Munthu uyu sachokera kwa Mulungu, chifukwa sasunga Sabata. Koma ena ananena, Munthu ali wochimwa akhoza bwanji kuchita zizindikiro zotere? Ndipo panali kutsutsana mwa iwo.