Yohane 7:40 - Buku Lopatulika Pamenepo ena a khamulo pakumva mau awa, ananena, Mneneriyo ndi uyu ndithu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamenepo ena a khamulo pakumva mau awa, ananena, Mneneriyo ndi uyu ndithu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamene khamu la anthu lidamva mau ameneŵa, ena mwa iwo ankati, “Zoonadi munthuyu ndiye Mneneri uja.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pakumva mawu ake, ena a anthuwo anati, “Zoonadi munthu uyu ndi mneneri.” |
Ndipo anamfunsa iye, Nanga bwanji? Ndiwe Eliya kodi? Nanena iye, Sindine iye. Ndiwe Mneneriyo kodi? Nayankha, Iai.
Chifukwa chake, anthu, poona chizindikiro chimene anachita, ananena, kuti, Ameneyo ndiye mneneri ndithu wakudzayo m'dziko lapansi.
Ndipo kunali kung'ung'udza kwambiri za Iye m'makamu a anthu; ena ananena, kuti, Ali wabwino; koma ena ananena, Iai, koma asocheretsa khamu la anthuwo.