Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Yohane 7:34 - Buku Lopatulika

Mudzafunafuna Ine, osandipeza; ndipo pomwe ndili Ine, inu simungathe kudzapo.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Mudzafunafuna Ine, osandipeza; ndipo pomwe ndili Ine, inu simungathe kudzapo.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Mudzandifunafuna, koma simudzandipeza. Ndipo kumene ndizikakhala Ine, inu simungathe kufikako.”

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Inu mudzandifunafuna koma simudzandipeza; ndipo kumene Ine ndili inu simungathe kubwera.”

Onani mutuwo



Yohane 7:34
12 Mawu Ofanana  

Adzamuka ndi zoweta zao zazing'ono ndi zazikulu kufunafuna Yehova: koma sadzampeza; Iye wadzibweza kuwachokera.


Pakuti ndinena kwa inu, Simudzandionanso Ine, kuyambira tsopano, kufikira mudzanena, Wolemekezedwa Iye amene akudza m'dzina la Ambuye.


Ndipo ngati ndipita kukakonzera inu malo, ndidzabweranso, ndipo ndidzalandira inu kwa Ine ndekha; kuti kumene kuli Ineko, mukakhale inunso.


Yesu ananena naye, Ine ndine njira, ndi choonadi, ndi moyo. Palibe munthu adza kwa Atate, koma mwa Ine.


Atate, amene mwandipatsa Ine, ndifuna kuti, kumene ndili Ine, iwonso akhale pamodzi ndi Ine; kuti ayang'anire ulemerero wanga, umene mwandipatsa Ine; pakuti munandikonda Ine lisanakhazikike dziko lapansi.


Mau awa amene ananena ndi chiyani, Mudzandifunafuna osandipeza Ine: ndipo pomwe ndili Ine, inu simungathe kudzapo?