Yohane 7:26 - Buku Lopatulika Ndipo taona amalankhula poyera, ndipo sanena kanthu kwa Iye. Kapena kodi akulu adziwa ndithu kuti ndiye Khristu ameneyo? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo taona amalankhula poyera, ndipo sanena kanthu kwa Iye. Kapena kodi akulu adziwa ndithu kuti ndiye Khristu ameneyo? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Si uyu akulankhula poyerayu, popandanso wonenapo kanthu! Kodi kapenatu ndiye kuti akuluakulu akuzindikiradi kuti ameneyu ndiye Mpulumutsi wolonjezedwa uja eti? Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Uyu ali apa, kuyankhula poyera, ndipo iwo sakunena kanthu kwa Iye. Kodi olamulira atsimikizadi kuti Iye ndi Khristu? |
Iye sadzalephera kapena kudololoka, kufikira atakhazikitsa chiweruzo m'dziko lapansi; ndipo zisumbu zidzalindira chilamulo chake.
Ndipo anatumiza kwa Iye ophunzira ao, pamodzi ndi Aherode, amene ananena, Mphunzitsi, tidziwa kuti muli woona, ndipo muphunzitsa njira ya Mulungu moona ndithu, ndipo simusamala munthu aliyense; pakuti simuyang'anira pa nkhope ya anthu.
Koma Afarisi ndi achilamulo anakaniza uphungu wa Mulungu kwa iwo okha, popeza sanabatizidwe ndi iye.
Kungakhale kotero, ambiri a mwa akulu anakhulupirira Iye; koma chifukwa cha Afarisi sanavomereze, kuti angaletsedwe m'sunagoge,
Yesu anayankha iye, Ine ndalankhula zomveka kwa dziko lapansi; ndinaphunzitsa Ine nthawi zonse m'sunagoge ndi mu Kachisi, kumene amasonkhana Ayuda onse; ndipo mobisika sindinalankhule kanthu.
Tiyeni, mukaone munthu, amene anandiuza zinthu zilizonse ndinazichita: ameneyu sali Khristu nanga?
Koma ambiri a m'khamu la anthu anakhulupirira Iye; ndipo ananena, Pamene Khristu akadza kodi adzachita zizindikiro zambiri zoposa zimene adazichita ameneyo?
Izi ananena atate wake ndi amake, chifukwa anaopa Ayuda; pakuti Ayuda adapangana kale, kuti ngati munthu aliyense adzamvomereza Iye kuti ndiye Khristu, akhale woletsedwa m'sunagoge.
Koma pakuona kulimbika mtima kwa Petro ndi Yohane, ndipo pozindikira kuti ndiwo anthu osaphunzira ndi opulukira, anazizwa ndipo anawazindikira, kuti adakhala pamodzi ndi Yesu.
ndi kuti unyinji wa abale mwa Ambuye, pokhulupirira m'zomangira zanga, alimbika mtima koposa kulankhula mau a Mulungu opanda mantha.