Yohane 7:24 - Buku Lopatulika Musaweruze monga maonekedwe, koma weruzani chiweruziro cholungama. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Musaweruze monga maonekedwe, koma weruzani chiweruziro cholungama. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Musamaweruza poyang'ana maonekedwe chabe, koma muziweruza molungama.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Musamaweruze potengera maonekedwe chabe, koma weruzani molungama.” |
Wokometsa mlandu wa wamphulupulu, ndi wotsutsa wolungama, onse awiriwa amnyansa Yehova.
Musamachita chisalungamo pakuweruza mlandu; usamavomereza munthu wosauka, kapena kulemekeza munthu womveka; uweruze mlandu wa munthu mnzako molungama.
Watero Yehova wa makamu, kuti, Weruzani chiweruzo choona, nimuchitire yense mnzake chifundo ndi ukoma mtima;
Kodi mupenyera zopenyeka pamaso? Ngati wina alimbika mwa yekha kuti ali wa Khristu, ayesere ichinso mwa iye yekha, kuti monga iye ali wa Khristu, koteronso ife.
Abale anga, pakuti muli nacho chikhulupiriro cha Ambuye wathu Yesu Khristu, Ambuye wa ulemerero, musakhale okondera ndi kusamala maonekedwe.
koma ngati musamala maonekedwe, muchita uchimo, ndipo mutsutsidwa ndi chilamulo monga olakwa.