Ngakhale bwenzi langa lenileni, amene ndamkhulupirira, ndiye amene adadyako mkate wanga, anandikwezera chidendene chake.
Yohane 6:71 - Buku Lopatulika Koma adanena za Yudasi, mwana wa Simoni Iskariote, pakuti iye ndiye amene akampereka Iye, ali mmodzi wa khumi ndi awiri. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma adanena za Yudasi, mwana wa Simoni Iskariote, pakuti iye ndiye amene akampereka Iye, ali mmodzi wa khumi ndi awiri. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ankanena Yudasi, mwana wa Simoni Iskariote. Ngakhale anali mmodzi mwa ophunzira aja khumi ndi aŵiri, koma ndiye amene analikudzapereka Yesu kwa adani ake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (Iye amanena Yudasi, mwana wa Simoni Isikarioti amene ngakhale anali mmodzi mwa khumi ndi awiriwo, anali woti adzamupereka). |
Ngakhale bwenzi langa lenileni, amene ndamkhulupirira, ndiye amene adadyako mkate wanga, anandikwezera chidendene chake.
Ndipo maina ao a atumwiwo khumi ndi awiri ndi awa: woyamba Simoni wotchedwa Petro, ndi Andrea mbale wake; Yakobo mwana wa Zebedeo, ndi Yohane mbale wake;
Ndipo Yudasi Iskariote, ndiye mmodzi wa khumi ndi awiriwo, anachoka napita kwa ansembe aakulu, kuti akampereke Iye kwa iwo.
Ndipo pokhala pamgonero, mdierekezi adatha kuika mu mtima wake wa Yudasi mwana wa Simoni Iskariote, kuti akampereke Iye,
Ndipo Yesu anayankha, Ndi iyeyu, amene Ine ndidzamsunsira nthongo ndi kumpatsa. Pamenepo, m'mene anasunsa nthongo anaitenga naipatsa Yudasi mwana wa Simoni Iskariote.
Koma Tomasi, mmodzi wa khumi ndi awiriwo, wotchedwa Didimo, sanakhale nao pamodzi, pamene Yesu anadza.
Koma pali ena mwa inu amene sakhulupirira. Pakuti Yesu anadziwa poyamba amene ali osakhulupirira, ndi amene adzampereka.
Yesu anayankha iwo, Kodi sindinakusankhani khumi ndi awiri, ndipo mwa inu mmodzi ali mdierekezi?
ameneyo, woperekedwa ndi uphungu woikidwa ndi kudziwiratu kwa Mulungu, inu mwampachika ndi kumupha ndi manja a anthu osaweruzika;
Pakuti pali anthu ena anakwawira m'tseri, ndiwo amene aja adalembedwa maina ao kale, kukalandira chitsutso ichi, anthu osapembedza, akusandutsa chisomo cha Mulungu wathu chikhale chilakolako chonyansa, nakaniza Mfumu wayekha, ndi Ambuye wathu, Yesu Khristu.