Ndipo umene ndiwo umboni wa Yohane, pamene Ayuda anatuma kwa iye ansembe ndi Alevi a ku Yerusalemu akamfunse iye, Ndiwe yani?
Yohane 6:52 - Buku Lopatulika Pamenepo Ayuda anatetana wina ndi mnzake ndi kunena, Akhoza bwanji ameneyu kutipatsa ife kudya thupi lake? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamenepo Ayuda anatetana wina ndi mnzake ndi kunena, Akhoza bwanji ameneyu kutipatsa ife kudya thupi lake? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamenepo Ayuda aja adayamba kukangana okhaokha, ankati, “Munthu ameneyu angathe bwanji kutipatsa thupi lake kuti tidye?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka Ayuda anayamba kutsutsana kwambiri pakati pawo kuti, “Kodi munthu uyu angathe kutipatsa bwanji thupi lake kuti tidye?” |
Ndipo umene ndiwo umboni wa Yohane, pamene Ayuda anatuma kwa iye ansembe ndi Alevi a ku Yerusalemu akamfunse iye, Ndiwe yani?
Nikodemo ananena kwa Iye, Munthu akhoza bwanji kubadwa atakalamba? Kodi akhoza kulowanso m'mimba ya amake ndi kubadwa?
Mkaziyo ananena ndi Iye, Ambuye, mulibe chotungira madzi, ndi chitsime chili chakuya; ndipo mwatenga kuti madzi amoyo?
Chifukwa chake Ayuda anang'ung'udza za Iye, chifukwa anati, Ine ndine mkate wotsika Kumwamba.
Pamenepo ambiri a ophunzira ake, pakumva izi, anati, Mau awa ndi osautsa; akhoza kumva awa ndani?
Ena pamenepo mwa Afarisi ananena, Munthu uyu sachokera kwa Mulungu, chifukwa sasunga Sabata. Koma ena ananena, Munthu ali wochimwa akhoza bwanji kuchita zizindikiro zotere? Ndipo panali kutsutsana mwa iwo.
Ndipo pamene anamva za kuuka kwa akufa ena anaseka pwepwete; koma ena anati, Tidzakumvanso za chimenechi.
Koma munthu wa chibadwidwe cha umunthu salandira za Mzimu wa Mulungu: pakuti aziyesa zopusa; ndipo sangathe kuzizindikira, chifukwa ziyesedwa mwauzimu.