Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Yohane 6:5 - Buku Lopatulika

Pamenepo Yesu, pokweza maso ake, ndi kuona kuti khamu lalikulu lilinkudza kwa Iye, ananena kwa Filipo, Tidzagula kuti mikate kuti adye awa?

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Pamenepo Yesu, pokweza maso ake, ndi kuona kuti khamu lalikulu lilinkudza kwa Iye, ananena kwa Filipo, Tidzagula kuti mikate kuti adye awa?

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Pamene Yesu adayang'ana, adaona khamu lalikulu la anthu lija likudza kwa Iye. Tsono Iye adafunsa Filipo kuti, “Kodi tingakagule kuti chakudya chodyetsa anthu onseŵa?”

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yesu atakweza maso ndi kuona gulu lalikulu la anthu likubwera kwa Iye, anati kwa Filipo, “Kodi tingagule kuti buledi kuti anthu awa adye?”

Onani mutuwo



Yohane 6:5
14 Mawu Ofanana  

Ndidzaiona kuti nyama yakuwapatsa anthu awa onse? Pakuti amalirira ine, ndi kuti, Tipatseni nyama, tidye.


Ndipo ophunzira ananena kwa Iye, Tiione kuti mikate yotere m'chipululu yakukhutitsa unyinji wotere wa anthu?


Ndipo anachokera m'ngalawa kunka kumalo achipululu padera.


Ndipo atabwera atumwi, anamfotokozera Iye zonse anazichita. Ndipo Iye anawatenga, napatuka nao pa okha kunka kumzinda dzina lake Betsaida.


M'mawa mwake anafuna kutuluka kunka ku Galileya, napeza Filipo. Ndipo Yesu ananena naye, Tsata Ine.


Koma Filipo anali wa ku Betsaida, mzinda wa Andrea ndi Petro.


Filipo anapeza Natanaele, nanena naye, Iye amene Mose analembera za Iye m'chilamulo, ndi aneneri, tampeza, ndiye Yesu mwana wa Yosefe wa ku Nazarete.


Natanaele anati kwa iye, Ku Nazarete nkutha kuchokera kanthu kabwino kodi? Filipo ananena naye, Tiye ukaone.


Natanaele ananena naye, Munandidziwira kuti? Yesu anayankha nati kwa iye, Asanakuitane Filipo, pokhala iwe pansi pa mkuyu paja, ndinakuona iwe.


Kodi simunena inu, kuti, Yatsala miyezi inai, ndipo kudza kumweta? Onani ndinena kwa inu, Kwezani maso anu, nimuyang'ane m'minda, kuti mwayera kale kufikira kumweta.