Yohane 6:41 - Buku Lopatulika Chifukwa chake Ayuda anang'ung'udza za Iye, chifukwa anati, Ine ndine mkate wotsika Kumwamba. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chifukwa chake Ayuda anang'ung'udza za Iye, chifukwa anati, Ine ndine mkate wotsika Kumwamba. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamenepo Ayudawo adayamba kung'ung'udza chifukwa Yesu adaati, “Ine ndine chakudya chotsika kuchokera Kumwamba.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamenepo Ayuda anayamba kungʼungʼudza chifukwa anati, “Ine ndine chakudya chotsika kuchokera kumwamba.” |
Ndipo m'mene anachiona anadandaula onse, nanena, Analowa amchereze munthu ali wochimwa.
Ndipo Afarisi ndi alembi ao anang'ung'udza kwa ophunzira ake, nanena, kuti, Bwanji inu mukudya ndi kumwa pamodzi ndi anthu amisonkho ndi ochimwa?
Ndipo umene ndiwo umboni wa Yohane, pamene Ayuda anatuma kwa iye ansembe ndi Alevi a ku Yerusalemu akamfunse iye, Ndiwe yani?
Pakuti mkate wa Mulungu ndiye wakutsika kuchokera Kumwamba ndi kupatsa moyo kwa dziko lapansi.
Mkate wotsika Kumwamba ndi umenewu: si monga makolowo, anadya namwalira; iye wakudya mkate umene adzakhala ndi moyo nthawi zonse.
Pamenepo ambiri a ophunzira ake, pakumva izi, anati, Mau awa ndi osautsa; akhoza kumva awa ndani?
Ndipo kunali kung'ung'udza kwambiri za Iye m'makamu a anthu; ena ananena, kuti, Ali wabwino; koma ena ananena, Iai, koma asocheretsa khamu la anthuwo.
Amenewo ndiwo odandaula, oderera, akuyenda monga mwa zilakolako zao (ndipo pakamwa pao alankhula zazikuluzikulu), akutama anthu chifukwa cha kupindula nako.