Ambiri amati, Adzationetsa chabwino ndani? Weramutsirani ife kuunika kwa nkhope yanu, Yehova.
Yohane 6:34 - Buku Lopatulika Pamenepo anati kwa Iye, Ambuye, tipatseni ife mkate umene nthawi zonse. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamenepo anati kwa Iye, Ambuye, tipatseni ife mkate umene nthawi zonse. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Apo anthuwo adapempha Yesu kuti, “Ambuye, muzitipatsa chakudya chimenecho masiku onse.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iwo anati, “Ambuye, kuyambira tsopano muzitipatsa buledi ameneyu.” |
Ambiri amati, Adzationetsa chabwino ndani? Weramutsirani ife kuunika kwa nkhope yanu, Yehova.
Mkaziyo ananena kwa Iye, Ambuye, ndipatseni madzi amene, kuti ndisamve ludzu, kapena ndisadze kuno kudzatunga.
Yesu anayankha iwo nati, Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Mundifuna Ine, si chifukwa munaona zizindikiro, koma chifukwa munadya mkate, nimunakhuta.
Mulungu Atate wa Ambuye Yesu, Iye amene alemekezeka kunthawi yonse, adziwa kuti sindinama.