natenga mikateyo isanu ndi iwiri ndi nsombazo; nayamika Mulungu, nanyema, napatsa kwa ophunzira, ndi ophunzira kwa anthu.
Yohane 6:23 - Buku Lopatulika koma zinachokera ngalawa zina ku Tiberiasi, pafupi pamalo pomwe adadyapo mkate m'mene Ambuye Yesu adayamika; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 koma zinachokera ngalawa zina ku Tiberiasi, pafupi pa malo pomwe adadyapo mkate m'mene Ambuye Yesu adayamika; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Komabe zombo zina zochokera ku Tiberiasi zidafika pafupi ndi malo amene anthu aja adaadyera chakudya Ambuye atayamika Mulungu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka mabwato ena ochokera ku Tiberiya anafika pafupi ndi pamalo pamene anthu anadya buledi Ambuye atayamika. |
natenga mikateyo isanu ndi iwiri ndi nsombazo; nayamika Mulungu, nanyema, napatsa kwa ophunzira, ndi ophunzira kwa anthu.
Ndipo pamene Ambuye anamuona, anagwidwa ndi chifundo chifukwa cha iye, nanena naye, Usalire.
Ndipo Yohane anaitana awiri a ophunzira ake, nawatuma kwa Ambuye, nanena, Kodi ndinu wakudzayo, kapena tiyang'anire wina?
Zitapita izi anachoka Yesu kunka kutsidya lija la nyanja ya Galileya, ndiyo ya Tiberiasi.