Yohane 6:18 - Buku Lopatulika Ndipo nyanja inalikuuka chifukwa cha mphepo yaikulu yakuombako. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo nyanja inalikuuka chifukwa cha mphepo yaikulu yakuombako. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Komanso nyanja idaavwanduka, chifukwa mphepo inkaomba kwambiri. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mphepo yamphamvu inawomba ndipo nyanja inalusa. |
Akweza mitambo ichokere ku malekezero a dziko lapansi; ang'animitsa mphezi zidzetse mvula; atulutsa mphepo mosungira mwake.
Koma pomwepo ngalawa idafika pakati pa nyanja, yozunzika ndi mafunde; pakuti mphepo inadza mokomana nao.
ndipo pamene adalowa m'ngalawa, analikuoloka nyanja kunka ku Kapernao. Ndipo kutada pamenepo, koma Yesu asanadze kwa iwo.
Ndipo pamene adapalasa monga mastadiya makumi awiri ndi asanu kapena makumi atatu, anaona Yesu alikuyenda panyanja, ndi kuyandikira ngalawa; ndipo anachita mantha.