Yohane 6:13 - Buku Lopatulika Pomwepo anasonkhanitsa, nadzaza madengu khumi ndi awiri ndi makombo a mikate isanuyo yabarele, amene anatsalira anadyawo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pomwepo anasonkhanitsa, nadzaza madengu khumi ndi awiri ndi makombo a mikate isanuyo yabarele, amene anatsalira anadyawo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adatoladi zotsala zonse za buledi msanu uja, nadzaza madengu khumi ndi aŵiri. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho iwo anasonkhanitsa makombo nadzaza madengu khumi ndi awiri. |
Ndipo Amaziya anati kwa munthu wa Mulungu, Koma nanga titani nao matalente zana limodzi ndinapatsa ankhondo a Israele? Nati munthu wa Mulungu, Yehova ali nazo zoposa izi kukupatsani.
Ndipo anadya onse, nakhuta; ndipo anatola makombo otsala, nadzala madengu khumi ndi iwiri.
Pali mnyamata pano, amene ali nayo mikate isanu yabarele, ndi tinsomba tiwiri; koma nanga izi zikwanira bwanji ambiri otere?
Koma Mulungu wanga adzakwaniritsa chosowa chanu chilichonse monga mwa chuma chake mu ulemerero mwa Khristu Yesu.