Nanena naonso, Mukani, mukadye zonona, mukamwe zozuna, nimumtumizire gawo lake iye amene sanamkonzeretu kanthu; chifukwa lero ndilo lopatulikira Ambuye wathu; ndipo musamachita chisoni; pakuti chimwemwe cha Yehova ndicho mphamvu yanu.
Yohane 6:12 - Buku Lopatulika Ndipo pamene adakhuta, Iye ananena kwa ophunzira ake, Sonkhanitsani makombo kuti kasatayike kanthu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo pamene adakhuta, Iye ananena kwa ophunzira ake, Sonkhanitsani makombo kuti kasatayike kanthu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Anthu onsewo atakhuta, Yesu adauza ophunzira ake kuti, “Tolani zotsala kuti pasatayikepo kanthu.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo atakhuta, Iye anati kwa ophunzira ake, “Tolani zotsala kuti pasawonongeke kanthu.” |
Nanena naonso, Mukani, mukadye zonona, mukamwe zozuna, nimumtumizire gawo lake iye amene sanamkonzeretu kanthu; chifukwa lero ndilo lopatulikira Ambuye wathu; ndipo musamachita chisoni; pakuti chimwemwe cha Yehova ndicho mphamvu yanu.
Ndipo analanda mizinda yamalinga, ndi dziko la zonona, nalandira zikhale zaozao nyumba zodzala ndi zokoma zilizonse, zitsime zokumbidwa, minda yampesa, ndi minda ya azitona, ndi mitengo yambiri yazipatso; nadya iwo, nakhuta, nanenepa, nakondwera nako kukoma kwanu kwakukulu.
Ndipo pakupita masiku owerengeka mwana wamng'onoyo anasonkhanitsa zonse, napita ulendo wake kudziko lakutali; ndipo komweko anamwaza chuma chake ndi makhalidwe a chitayiko.
Ndipo Iye ananenanso kwa ophunzira ake, Panali munthu mwini chuma, anali ndi kapitao wake; ndipo ameneyu ananenezedwa kwa iye kuti alikumwaza chuma chake.