Yohane 5:41 - Buku Lopatulika Ulemu sindiulandira kwa anthu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ulemu sindiulandira kwa anthu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Sindikufunafuna ulemu wa anthu ai. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Ine sindilandira ulemu kuchokera kwa anthu |
Mungathe inu bwanji kukhulupirira, popeza mulandira ulemu wina kwa mnzake ndipo ulemu wakuchokera kwa Mulungu yekha simuufuna?
Pamenepo Yesu, pozindikira kuti alikufuna kudza kudzamgwira Iye, kuti amlonge ufumu, anachokanso kunka kuphiri pa yekha.
Iye wolankhula zochokera kwa iye yekha afuna ulemu wa mwini yekha. Iye wakufuna ulemu wa Iye amene anamtuma, yemweyu ali woona, ndipo mwa Iye mulibe chosalungama.
Yesu anayankha, Ngati Ine ndidzilemekeza ndekha, ulemerero wanga uli chabe; Atate wanga ndiye wondilemekeza Ine; amene munena za Iye, kuti ndiye Mulungu wanu;
kapena sitinakhale ofuna ulemerero wa kwa anthu, kapena kwa inu, kapena kwa ena, tingakhale tinali nayo mphamvu yakukulemetsani monga atumwi a Khristu.
Pakuti kudzachita ichi mwaitanidwa; pakutinso Khristu anamva zowawa m'malo mwanu, nakusiyirani chitsanzo kuti mukalondole mapazi ake;
Pakuti analandira kwa Mulungu Atate ulemu ndi ulemerero, pakumdzera Iye mau otere ochokera ku ulemerero waukulu, Uyu ndi Mwana wanga wokondedwa, amene Ine ndikondwera naye;