Yohane 5:26 - Buku Lopatulika Pakuti monga Atate ali ndi moyo mwa Iye yekha, momwemonso anapatsa kwa Mwana kukhala ndi moyo mwa Iye yekha; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti monga Atate ali ndi moyo mwa Iye yekha, momwemonso anapatsa kwa Mwana kukhala ndi moyo mwa Iye yekha; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Monga Atate ali gwelo la moyo, momwemonso adaika Mwana wake kuti nayenso akhale gwelo la moyo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pakuti monga Atate ali gwero la moyo, momwemonso anapereka mphamvu zopereka moyo mwa Mwana. |
Asanabadwe mapiri, kapena musanalenge dziko lapansi, ndi lokhalamo anthu, inde, kuyambira nthawi yosayamba kufikira nthawi yosatha, Inu ndinu Mulungu.
Ndipo Mulungu anati kwa Mose, INE NDINE YEMWE NDILI INE. Anatinso, Ukatero ndi ana a Israele, INE NDINE wandituma kwa inu.
Koma Yehova ndiye Mulungu woona; ndiye Mulungu wamoyo, mfumu yamuyaya; pa mkwiyo wake dziko lapansi lidzanthunthumira, ndi amitundu sangapirire ukali wake.
Palibe wina andichotsera uwu, koma ndiutaya Ine ndekha. Ndili nayo mphamvu yakuutaya, ndi mphamvu ndili nayo yakuutenganso; lamulo ili ndinalandira kwa Atate wanga.
Yesu anati kwa iye, Ine ndine kuuka ndi moyo: wokhulupirira Ine, angakhale amwalira, adzakhala ndi moyo;
ndipo yense wakukhala ndi moyo, nakhulupirira Ine, sadzamwalira nthawi yonse. Kodi ukhulupirira ichi?
Katsala kanthawi, ndipo dziko lapansi silindionanso Ine; koma inu mundiona; popeza Ine ndili ndi moyo inunso mudzakhala ndi moyo.
Yesu ananena naye, Ine ndine njira, ndi choonadi, ndi moyo. Palibe munthu adza kwa Atate, koma mwa Ine.
Yesu anayankha nati kwa iye, Ukadadziwa mtulo wa Mulungu, ndi Iye amene alinkunena ndi iwe, Undipatse Ine ndimwe; ukadapempha Iye, ndipo akadakupatsa madzi amoyo.
Monga Atate wamoyo anandituma Ine, ndipo Inenso ndili ndi moyo chifukwa cha Atate; momwemo wondidya Ine, iyeyu adzakhala ndi moyo chifukwa cha Ine.
satumikiridwa ndi manja a anthu, monga wosowa kanthu, popeza Iye mwini apatsa zonse moyo ndi mpweya ndi zinthu zonse;
Koteronso kwalembedwa, Munthu woyamba, Adamu, anakhala mzimu wamoyo. Adamu wotsirizayo anakhala mzimu wakulenga moyo.
Ndipo kwa Mfumu yosatha, yosavunda, yosaoneka, Mulungu wa yekha, ukhale ulemu ndi ulemerero, kufikira nthawi za nthawi. Amen.
amene Iye yekha ali nao moyo wosatha, wakukhala m'kuunika kosakhozeka kufikako; amene munthu sanamuone, kapena sangathe kumuona; kwa Iye kukhale ulemu ndi mphamvu yosatha. Amen.
koma pakutha pake pa masiku ano analankhula ndi ife ndi Mwana amene anamuika wolowa nyumba wa zonse, mwa Iyenso analenga maiko ndi am'mwamba omwe;
Ndipo anati kwa ine, Zatha. Ine ndine Alefa ndi Omega, Woyamba ndi Wotsiriza. Kwa iye wakumva ludzu ndidzampatsa amwe kukasupe wa madzi a moyo kwaulere.
Ndipo anandionetsa mtsinje wa madzi a moyo, wonyezimira ngati krustalo, otuluka kumpando wachifumu wa Mulungu ndi wa Mwanawankhosa.
Ndipo Mzimu ndi mkwatibwi anena, Idzani. Ndipo wakumva anene, Idzani. Ndipo wakumva ludzu adze; iye wofuna, atenge madzi a moyo kwaulere.
chifukwa Mwanawankhosa wakukhala pakati pa mpando wachifumu adzawaweta, nadzawatsogolera ku akasupe a madzi amoyo, ndipo Mulungu adzawapukutira misozi yonse pamaso pao.