Pomwepo ananena Iye kwa munthuyo, Tansa dzanja lako. Ndipo iye analitansa, ndipo linabwezedwa lamoyo longa linzake.
Yohane 5:16 - Buku Lopatulika Ndipo chifukwa cha ichi Ayuda analondalonda Yesu, popeza anachita izo tsiku la Sabata. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo chifukwa cha ichi Ayuda analondalonda Yesu, popeza anachita izo tsiku la Sabata. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Popeza kuti linali tsiku la Sabata pamene Yesu adaachita zimenezi, Ayuda adayamba kumuvutitsa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo popeza Yesu amachita zinthu izi tsiku la Sabata, Ayuda anayamba kumulondalonda. |
Pomwepo ananena Iye kwa munthuyo, Tansa dzanja lako. Ndipo iye analitansa, ndipo linabwezedwa lamoyo longa linzake.
Ndipo umene ndiwo umboni wa Yohane, pamene Ayuda anatuma kwa iye ansembe ndi Alevi a ku Yerusalemu akamfunse iye, Ndiwe yani?
Kumbukirani mau amene Ine ndinanena kwa inu, Kapolo sali wamkulu ndi mbuye wake. Ngati anandilondalonda Ine, adzakulondalondani inunso; ngati anasunga mau anga, adzasunga anunso.
Chifukwa chake Ayuda ananena kwa wochiritsidwayo, Ndi Sabata, ndipo sikuloledwa kwa iwe kuyalula mphasa yako.
Koma wochiritsidwayo sanadziwe kuti anali ndani; pakuti Yesu anachoka kachetechete, popeza panali anthu aunyinji m'malo muja.
Koma Yesu anayankha iwo, Atate wanga amagwira ntchito kufikira tsopano, Inenso ndigwira ntchito.
Chifukwa cha ichi Ayuda anaonjeza kufuna kumupha, si chifukwa cha kuswa tsiku la Sabata kokha, komatu amatchanso Mulungu Atate wake wa Iye yekha; nadziyesera wolingana ndi Mulungu.