Ndipo m'mene Iye analowa mu Kachisi, ansembe aakulu ndi akulu a anthu anadza kwa Iye analikuphunzitsa, nanena, Muchita izi ndi ulamuliro wotani? Ndipo ndani anakupatsani ulamuliro wotere?
Yohane 5:12 - Buku Lopatulika Anamfunsa, Munthuyo ndani wonena ndi iwe, Yalula mphasa yako, nuyende? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Anamfunsa, Munthuyo ndani wonena ndi iwe, Yalula mphasa yako, nuyende? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Iwo adamufunsa kuti, “Munthuyo ndani amene wakuuza kuti unyamule mphasa yako, uyende?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamenepo anamufunsa iye kuti, “Kodi munthu ameneyo ndani amene wakuwuza kuti, ‘Nyamula mphasa yako ndipo yenda?’ ” |
Ndipo m'mene Iye analowa mu Kachisi, ansembe aakulu ndi akulu a anthu anadza kwa Iye analikuphunzitsa, nanena, Muchita izi ndi ulamuliro wotani? Ndipo ndani anakupatsani ulamuliro wotere?
Koma iyeyu anayankha iwo, Iye amene anandichiritsa, yemweyu anati kwa ine, Yalula mphasa yako, nuyende.
Koma wochiritsidwayo sanadziwe kuti anali ndani; pakuti Yesu anachoka kachetechete, popeza panali anthu aunyinji m'malo muja.
Pakuti ndiwachitira iwo umboni kuti ali ndi changu cha kwa Mulungu, koma si monga mwa chidziwitso.
Nanenana wina ndi mnzake, Wachita ichi ndani? Ndipo atafunafuna nafunsafunsa, anati, Gideoni, mwana wa Yowasi wachita ichi.
Ndipo Saulo anati, Musendere kuno, inu nonse akulu a anthu; kuti muzindikire ndi kuona m'mene muli choipa ichi lero.