Koma anati kwa iwo, Muwapatse chakudya ndinu. Koma anati, Ife tilibe mikate, koma isanu yokha, ndi nsomba ziwiri zokha; kapena timuke ife kukagulira anthu awa onse zakudya.
Yohane 4:8 - Buku Lopatulika Pakuti ophunzira ake adachoka kunka kumzinda kuti akagule chakudya. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti ophunzira ake adachoka kunka kumudzi kuti akagule chakudya. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nthaŵiyo nkuti ophunzira ake aja atakagula chakudya mu mzinda. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (Ophunzira ake nʼkuti atapita mʼmudzi kukagula chakudya). |
Koma anati kwa iwo, Muwapatse chakudya ndinu. Koma anati, Ife tilibe mikate, koma isanu yokha, ndi nsomba ziwiri zokha; kapena timuke ife kukagulira anthu awa onse zakudya.
Ndipo pamenepo anadza ophunzira ake; nazizwa kuti analinkulankhula ndi mkazi; koma panalibe wina anati, Mufuna chiyani? Kapena, mulankhula naye chiyani?
Ndipo m'mzinda muja anthu Asamariya ambiri anamkhulupirira Iye chifukwa cha mau a mkazi, wochita umboniyo, kuti, Anandiuza ine zinthu zilizonse ndinazichita.
Chifukwa chake anadza kumzinda wa Samariya, dzina lake Sikari, pafupi pa kadziko kamene Yakobo adapatsa mwana wake Yosefe;
Kunali ngati ora lachisanu ndi chimodzi. Kunadza mkazi wotuluka mu Samariya kudzatunga madzi. Yesu ananena naye, Undipatse Ine ndimwe.