Yohane 4:53 - Buku Lopatulika Chifukwa chake atateyo anadziwa kuti ndi ora lomwelo limene Yesu anati kwa iye, Mwana wako ali ndi moyo; ndipo anakhulupirira iye yekha ndi a pa banja lake onse. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chifukwa chake atateyo anadziwa kuti ndi ora lomwelo limene Yesu anati kwa iye, Mwana wako ali ndi moyo; ndipo anakhulupirira iye yekha ndi a pa banja lake onse. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Bamboyo adazindikira kuti inali nthaŵi yomwe Yesu adaamuuza kuti, “Mwana wanu wachira.” Tsono iye adakhulupirira pamodzi ndi onse a m'banja mwake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo bamboyo anazindikira kuti iyi inali nthawi yomweyo imene Yesu anati kwa iye, “Mwana wako adzakhala ndi moyo.” Choncho iye ndi onse a pa banja lake anakhulupirira. |
Ndipo Yesu anati kwa kenturiyoyo, Pita, kukhale kwa iwe monga unakhulupirira. Ndipo anachiritsidwa mnyamatayo nthawi yomweyo.
Ndipo Yesu anati kwa iye, Lero chipulumutso chagwera nyumba iyi, popeza iyenso ndiye mwana wa Abrahamu.
Ndipo m'mene analikutsika, akapolo ake anakomana naye, nanena, kuti, Mwana wanu ali ndi moyo.
Chifukwa chake anawafunsa ora lake anayamba kuchiralo. Pamenepo anati kwa iye, kuti, Dzulo, ora lachisanu ndi chiwiri malungo anamsiya.
Pamene anabatizidwa iye ndi a pabanja pake anatidandaulira ife, kuti, Ngati mwandiyesera ine wokhulupirika kwa Ambuye, mulowe m'nyumba yanga, mugone m'menemo. Ndipo anatiumiriza ife.
Ndipo anakwera nao kunka kunyumba kwake, nawakhazikira chakudya, nasangalala kwambiri, pamodzi ndi a pabanja pake, atakhulupirira Mulungu.
Ndipo Krispo, mkulu wa sunagoge, anakhulupirira Ambuye, ndi apabanja ake onse; ndipo Akorinto ambiri anamva, nakhulupirira, nabatizidwa.
Pakuti lonjezano lili kwa inu, ndi kwa ana anu, ndi kwa onse akutali, onse amene Ambuye Mulungu wathu adzaitana.