Ndipo iwo anakhumudwa chifukwa cha Iye. Koma Yesu anati kwa iwo, Mneneri sakhala wopanda ulemu koma kudziko la kwao ndiko, ndi kubanja kwake.
Yohane 4:44 - Buku Lopatulika Pakuti Yesu mwini anachita umboni kuti, Mneneri alibe ulemu m'dziko la kwao. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti Yesu mwini anachita umboni kuti, Mneneri alibe ulemu m'dziko la kwao. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mwiniwakeyo anali atanena kuti, “Mneneri, anthu akwao samchitira ulemu.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (Tsopano Yesu mwini ananena kale kuti mneneri salandira ulemu mʼdziko lake). |
Ndipo iwo anakhumudwa chifukwa cha Iye. Koma Yesu anati kwa iwo, Mneneri sakhala wopanda ulemu koma kudziko la kwao ndiko, ndi kubanja kwake.
Ndipo Yesu ananena kwa iwo, Mneneri sakhala wopanda ulemu, koma m'dziko la kwao ndimo, ndi pakati pa abale ake, ndi m'nyumba yake.
Ndipo Iye anati, Indetu, ndinena kwa inu, kuti, Palibe mneneri alandirika kudziko la kwao.